Revelation 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adayenda pa dziko lonse lapansi, nazinga misasa ya anthu a Mulungu, ndi mzinda umene Mulungu amaukonda. Koma moto udatsika kuchokera Kumwamba nkudzaŵaononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.