Revelation 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziŵiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi aŵiri, ndipo pa zitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nukhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi maina olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, unali ndi zipata khumi ndi ziwiri, ndipo panali angelo khumi ndi awiri. Pa chipata chilichonse panayima mngelo. Pa chipata chilichonse panalembedwa dzina la fuko la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nukhala nalo linga lalikuru ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi mama olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israyeli;