Revelation 21:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzindawo unali wolingana ponseponse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake munali chimodzimodzi. Mngelo uja adayesa chozungulira mzindawo ndi ndodo yake ija, napeza kuti kutalika kwake kunali makilomita 2,200. M'litali mwake, m'mimba mwake ndi msinkhu wake, zonse zinali zolingana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mzinda ukhala waphwamphwa; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzindawo unamangidwa mofanana kutalika kwake, mulitali ndi mulifupi munali mofanana. Anayeza mzindawo ndi ndodo ija ndipo anapeza kuti mulitali, mulifupi ndi msinkhu wake kutalika kwake kunali makilomita 2,200.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa; utali wace ulingana ndi kupingasa kwace: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wace, ndi kupingasa kwace, ndi kutalika kwace zilingana.