Revelation 21:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira;
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundumitundu; maziko oyamba, ndi yaspi; achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinai, ndi smaragido;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maziko a mpanda wa mzindawo anali okongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali ya mtundu uliwonse. Maziko oyamba anali yasipa, achiwiri anali safiro, achitatu ndi kalikedo, achinayi ndi simaragido,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu; mazikooyamba, ndi yaspi; aciwiri, ndi safiro; acitatu, ndi kalikedo; acinai, ndi smaragido;