Revelation 21:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wace.