Revelation 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamva mau akuru ocokera ku mpando wacifumu, ndi kunena Taonani, cihema ca Mulungu ciri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ace, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;