Revelation 21:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri yodzaza ndi miliri isanu ndi iŵiri yotsiriza ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno, ndikakuwonetse mkwati, mkazi wa Mwanawankhosa uja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja, anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri anandiwuza kuti, “Bwera, ine ndidzakuonetsa mkwatibwi wa Mwana Wankhosa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu Ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.