Revelation 22:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mngelo uja adandiwonetsa mtsinje wa madzi opatsa moyo. Mtsinjewo madzi ake anali onyezimira ngati galasi, ndipo unkachokera ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, oturuka ku mpando wacifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawarikhosa.