Revelation 22:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Unkayenda pakati pa mseu wamumzinda uja. Pa mbali zonse ziŵiri za mtsinje panali mtengo wopatsa moyo. Mtengowo umabala zipatso khumi ndi kaŵiri pa chaka, kamodzi mwezi uliwonse, ndipo masamba ake ndi ochiritsa anthu a mitundu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakati pa khwalala lace, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lace lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zace mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuciritsa nao amitundu.