Revelation 22:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mngelo uja adandiwuza kuti, “Mau aŵa ndi oona ndiponso oyenera kuŵakhulupirira. Ndipo Ambuye Mulungu amene amalankhulitsa aneneri, adatuma mngelo wao kuti aonetse atumiki ao zimene zidzachitike posachedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wace kukaonetsera akapolo ace zimene ziyenera kucitika msanga.