Revelation 3:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Sardi umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa amene amalamulira mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri ija, ndi nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zili m'manja mwakezi. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti muli ndi mbiri yoti ndinu amoyo, chonsecho ndinu akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sarde lemba: Izi anena iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi riwiri: Ndidziwa nchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.