Revelation 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye amene alakika adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye amene alakika adzambveka motero zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lace m'buku la moyo, ndipo ndidzambvomereza dzina lace pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ace.