Revelation 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidziwa nchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.