Revelation 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alipo ena a mpingo wa Satana, amene sali Ayuda, koma amanama kuti ndi Ayuda. Iwoŵa ndidzaŵabweretsa kwa inu kuti adzadzigwetse kumapazi kwanu. Pamenepo adzadziŵa kuti ndimakukondani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ndikupatsa ena oturuka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.