Revelation 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona pakhomo potsekuka Kumwamba. Ndipo ndidamva wina akulankhula nane ndi liwu lomwe ndidaamva poyamba lija, limene linkamveka ngati kulira kwa lipenga. Adandiwuza kuti, “Bwera Kumwamba kuno, ndidzakuwonetse zimene ziyenera kuchitika bwino lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka m'Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, nditayangʼana patsogolo panga ndinaona khomo lotsekuka la kumwamba. Ndipo liwu lija ndinalimva poyamba lokhala ngati lipenga linati, “Bwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene zichitike zikatha izi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka m'Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga Iakulankhuia ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kucitika m'tsogolomo.