Revelation 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene zikuchitika zimenezi, Akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pamaso pa wokhala pa mpando wachifumuyo, ndi kumpembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Ndipo amaponya pansi zisoti zao zaufumu patsogolo pa mpando wachifumuwo ndi kunena kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa iye wakukhala pa mpando wacifumu, namlambira iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao ku mpando wacifumu, ndi kunena,