Revelation 4:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mu mpando wachifumu munkatuluka mphezi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando womwewo pankayaka miyuni isanu ndi iŵiri, ndiye kuti mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mu mpando wacifumu mudaturuka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za mota zoyaka ku mpando wacifumu, ndiyo Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;