Revelation 4:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patsogolo pake panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira. Pakatimpakati, pozungulira mpando wachifumu uja, panali Zamoyo zinai, zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo. Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ku mpandowo, ngati nyanja, yamandala yonga krustalo; ndipopakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzaia ndi maso kutsogolo indi kumbuyo.