Revelation 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chamoyo choyamba chinkaoneka ngati mkango, chachiŵiri ngati ng'ombe, chachitatu chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo chachinai chinkaoneka ngati chiwombankhanga chouluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang'ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo camoyo coyamba cinafanana nao mkango, ndi camoyo caciwiri cinafanana ndi mwana wa ng'ombe, ndi camoyo cacitatu cinali nayo nkhope yace ngati ya munthu, ndi camoyo cacinai cidafanana ndi ciombankhanga cakuuluka.