Revelation 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona buku m'dzanja lamanja la wokhala pa mpando wachifumu uja. Bukulo linali lolembedwa m'kati ndi kumbuyo komwe, ndipo linali lomatidwa ndi zimatiro zisanu ndi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la iye wakukhala pa mpando wacifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwace, losindikizika ndi zizindikilo zisanu ndi ziwiri.