Revelation 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona namtindi wa angelo zikwizikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wacifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kucurukitsa zikwi khumi ndi zikwiza zikwi;