Revelation 5:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, kufikira nthawi za nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti, “Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa, kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo colengedwa ciri conse ciri m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndinazimva zirikunena, Kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale ciyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthawi za nthawi.