Revelation 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pakati pa mpando wachifumu uja ndi Zamoyo zinai zija ndiponso Akuluakulu 24 aja. Mwanawankhosayo ankaoneka ngati wophedwa, ndipo anali ndi nyanga zisanu ndi ziŵiri ndiponso maso asanu ndi aŵiri. Masowo ndi Mizimu isanu ndi iŵiri ija ya Mulungu yotumidwa m'dziko lonse lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona pakati pa mpando wacifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akuru, Mwanawankhosa ali ciriri ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.