Revelation 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adalilandira, Zamoyo zinai zija, pamodzi ndi Akuluakulu 24 aja, zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosayo. Aliyense mwa Akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mikhate yagolide yodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a anthu a Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nao azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.