Revelation 6:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizimuyo idafuula mokweza mau kuti, “Ambuye, Inu ndinu Mfumu yathu yoyera ndi yoona. Mudzaŵalekerera mpaka liti osaŵaimba mlandu ndi kuŵalanga anthu aja okhala pansi pano amene adatipha?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anafuula ndi mau akulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anapfuula ndi mau akulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera cilango cifukwa ca mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?