Revelation 6:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo aliyense adapatsidwa mkanjo woyera, ndipo adamva mau akuti, “Bapumulani pang'ono mpaka chitakwanira chiŵerengero chathunthu cha atumiki anzanu ndi abale anu, amene nawonso ayenera kuphedwa monga inu nomwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.