Revelation 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi cimodzi, ndipo panali cibvomezi cacikuru; ndi dzuwa lidada bii longa ciguduli ca ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;