Revelation 6:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zake zosapsa, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zace zosapsya, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.