Revelation 6:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m'malo mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Thambo linachoka ngati amayalulira mphasa ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pa malo pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kumwamba kudacoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kucoka m'malo mwao.