Revelation 6:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mafumu a dziko lapansi, atsogoleri a dziko, akulu a ankhondo, anthu olemera, anthu amphamvu, akapolo onse ndi mfulu zonse, onsewo adakabisala m'mapanga ndi m'matanthwe am'mapiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mafumu a dziko, ndi akuru, ndi akazembe, ndi acuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;