Revelation 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo kavalo wina, wofiira, adatulukira. Wokwerapo wake adaalandira mphamvu zothira nkhondo pa dziko lapansi, kuti anthu aziphana. Choncho adampatsa lupanga lalikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakucotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikuru.