Revelation 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachitatu. Ndipo ndidamva Chamoyo chachitatu chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo wakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m'manja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu nichinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacitatu, ndinamva camoyo cacitatu nicinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lace.