Revelation 6:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nditayang'ana, ndidaona kavalo wotuŵa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa, ndipo Malo a anthu akufa ankamutsata pambuyo. Aŵiriwo adaalandira ulamuliro pa chimodzi mwa zigawo zinai za dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi nkhondo, njala, nthenda, ndi zilombo zolusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wotuwa! Wokwerapo wake dzina lake linali Imfa ndipo Hade inali kumutsatira pambuyo pake. Anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi kuti aphe ndi lupanga, njala, mliri, ndi zirombo zakuthengo za mʼdziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.