Revelation 6:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatha izi, Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu. Ndipo ndidaona kunsi kwa guwa lansembe mizimu ya anthu amene adaphedwa chifukwa cha kulalika mau a Mulungu, ndiponso chifukwa chochitira mauwo umboni wamphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adamasula cizindikilo cacisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa cifukwa ca mau a Mulungu, ndi cifukwa ca umboni umene anali nao: