Revelation 7:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona angelo anai ataimirira pa mbali zinai za dziko lapansi. Anali atagwira mphepo zinai za dziko lapansi kuti ndi imodzi yomwe isaombe pa dziko, kapena pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha izi ndinaona angelo anai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi ndinao na angelo anai alinkuimirira pa ngondya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uli wonse.