Revelation 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwaine, Iwo ndiwo akuturuka m'cisautso cacikuru; ndipo anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.