Revelation 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka ndidaona mngelo wina akukwera kuchokera kuvuma, ali ndi chidindo cha Mulungu wopatsa moyo. Mokweza mau adafuulira angelo anai aja amene Mulungu adaaŵapatsa mphamvu yoonongera dziko ndi nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau akulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kucokera poturuka dzuwa, ali naco cizindikilo ca Mulungu wamoyo: ndipo anapfuula ndi mau akuru kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,