Revelation 8:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wachitatu adaliza lipenga lake. Atatero chinyenyezi choyaka ngati muuni chidagwa kuchokera kuthambo. Chidagwera pa chimodzi mwa zigawo zitatu za mitsinje, ndi pa akasupe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachitatu anayimba lipenga lake, ndipo nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muni inachoka kumwamba nigwera pa gawo limodzi la magawo atatu a mitsinje ndi pa akasupe amadzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaomba mngelo wacitatu, ndipo idagwa kucokera kumwamba nyenyezi yaikuru, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;