Revelation 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinyenyezicho dzina lake ndi “Kuŵaŵa”. Chimodzi mwa zigawo zitatu za madzi chidasanduka choŵaŵa, mwakuti anthu ambiri adafa nawo madziwo chifukwa cha kuŵaŵa kwakeko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzina la nyenyeziyo ndi Chowawa. Gawo limodzi la magawo atatu a madzi anasanduka owawa ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha madzi owawawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo dzina lace la nyenyeziyo alicha Cowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka cowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti anasanduka owawa.