Revelation 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wachinai adaliza lipenga lake. Atatero chimodzichimodzi mwa zigawo zitatuzitatu za dzuŵa, za mwezi ndi za nyenyezi chidamenyedwa. Zitachitika zimenezi, chimodzi mwa zigawo zitatu za zonsezo chidada. Panalibenso kuŵala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachinayi anayimba lipenga lake, ndipo chimodzi cha zigawo zitatu za dzuwa, za mwezi ndi za nyenyezi zinamenyedwa kotero chimodzi mwa zitatu za zonsezi zinada. Panalibenso kuwala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngelo wacinai anaomba, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ace atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.