Revelation 8:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidayang'ana, ndipo ndidaona chiwombankhanga chikuuluka mu mlengalenga, ndipo ndidamva chikulira mokweza kuti, “Tsoka! Tsoka! Tsoka kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi, angelo atatu otsala aja akangoliza malipenga ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayangʼananso ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chimene chinkawuluka mlengalenga kwambiri chikuyankhula mofuwula kuti, “Tsoka, Tsoka! Tsoka lalikulu kwa anthu okhala mʼdziko lapansi, angelo otsala aja akangoyimba malipenga awo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva ciombankhanga cirikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akuru, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padz'ko, cifukwa ca mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.