Revelation 8:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wina adabwera naimirira ku guwa lansembe ali ndi chofukizira chagolide. Adapatsidwa lubani wambiri kuti ampereke pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulungu pa guwa lagolide patsogolo pa mpando wachifumu uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala naco cotengera ca zofukiza cagolidi; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wacifumu.