Revelation 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mngeloyo adatenga chofukiziracho nachidzaza ndi moto wochokera ku guwa lija. Adachiponya pa dziko lapansi, ndipo nthaŵi yomweyo padachitika mabingu, phokoso, mphezi ndi chivomezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mngeloyo anatenga chofukizira nachidzaza ndi moto wochokera pa guwa lansembe ndi kuponya pa dziko lapansi ndipo nthawi yomweyo panachitika mabingu, phokoso, mphenzi ndi chivomerezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi mota wopara pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi cibvomezi.