Revelation 9:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'masomphenya momwemo, akavalowo ndidaŵaona motere: okwerapo ake adaavala malaya achitsulo apachifuwa a maonekedwe ofiira ngati moto, obiriŵira ngati utsi, ndi achikasu ngati miyala ya sulufure. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango, ndipo m'kamwa mwao munkatuluka moto, utsi ndi sulufure.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akavalo ndi okwerapo amene ndinaona mʼmasomphenya anga ankaoneka motere: Zovala za pachifukwa pawo zinali zofiira ngati moto, zobiriwira ngati utsi, ndi zachikasu ngati miyala ya sulufule. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango ndipo mʼkamwa mwawo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulfure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao muturuka moto ndi utsi ndi sulfure.