Revelation 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse chidaphedwa ndi miliri itatu iyi: wa moto, wa utsi ndi wa sulufure, zimene zinkatuluka m'kamwa mwa akavalo aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulufure, zotuluka m'kamwa mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gawo limodzi la magawo atatu a anthu linaphedwa ndi miliri yamoto, utsi ndi sulufule zimene zinkachoka mʼkamwa mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulfure, zoturuka m'kamwa mwao.