Revelation 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyenyeziyo idatsekula padzenjepo, ndipo padatuluka utsi wonga wam'ching'anjo. Dzuŵa ndi thambo zidada chifukwa cha utsi wotuluka m'dzenjewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m'chiphomphomo, ngati utsi wa ng'anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyenyeziyo itatsekula pa chidzenje chakuyacho panatuluka utsi ngati wochokera mʼngʼanjo yayikulu. Dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsi ochokera mʼdzenjemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatsegula pa dzenje la phompho; ndipo unakwera utsi woturuka m'dzenjemo, ngati utsi wa ng'anjo yaikuru; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, cifukwa ca utsiwo wa kudzenje,