Revelation 9:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa nchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolidi, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi amwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;