Romans 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, ndifuna kuti mudziŵe kuti kaŵirikaŵiri ndakhala ndikuganiza zobwera kwanuko, koma mpaka tsopano panali zina zondiletsa. Ndifuna kuti pakati panuponso ndidzagwire ntchito yoonetsa zipatso, monga zidachitikira pakati pa anthu enanso a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa kuti nthawi zambiri ndakhala ndikufuna zobwera kwanuko, koma mpaka pano pali zolepheretsa, ndi cholinga choti ndidzapezeko zipatso pakati panupo monga momwe ndakhala ndikuchitira pakati pa a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.