Romans 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti m'menemo caonetsedwa cilungamoca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro.