Romans 1:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wocokera Kumwamba, uonekera pa cisapembedzo conse ndi cosalungama ca anthu, amene akanikiza pansi coonadi m'cosalungama cao;